GROUNDNUT PRODUCTION GUIDE
- Prepare your land before
- Space your ridges from 75 – 90cm, and plant 1 seed per station at 10 cm apart. Make 2 rows on the ridge spaced at 30cm. Seed need around 80kg/ha or 32kg/acre.
- Keep the field weed free, especially the first six to eight weeks
- When your crop is flowering weed only by hand as using a hoe might disturb pegging.
- Make periodic check for maturity. Your mature pod will show black spot inside the shell.
- Harvest when most of your pods show maturity sign. Stook the nuts upside down on stacks to necessitate drying process
- Hand or machine shell when your nuts are thoroughly dry.
NOTE: Also seek technical advise from the agricultural extension staff of your area.
KALIMIDWE KA MBEWU YA MTEDZA.
- Sosani ndi kugalauza munda wanu usanafike mwedzi wa November.
- Konzani mizere yosachepera pa 75 komanso osapitilira 90cm.
- Bzalani mtedza umodzi pa mapando otalikirana 10cm mmikhwasa komanso mikhwasa iwiri pa mdzere umodzi.
- Munda mukhale mopanda udzu kwa masabata asanu ndi limodzi kapena asanu ndi atatu.
- Pa nthawi yomwe mbewu yayamba maluwa kusosela kuchitike podzulira kuopera kutsokoneza
- Yenderani mmunda mwanu kuona ngati mtedza wayamba kukhwima. Mtedza wokhwima umaonetsa madontho akuda mkati mwakhoko.
- Pamene makoko ambiri akuwonetsa dzidzindikiro zokhwima, yambamponi kuchotsa ndipo tembenuzani masangwe pa mulu kuti mtedza ukhale kudzuwa.
- Mbewu ikawuma bwino thotholani ndikuyanba kusenda ndi manja kapena ndi makina.
CHIDZIWITSO: Funsirani zoonjezera kuchokera kwa alangizi a mdera lanu.